Chilankhulo cha Chichewa
Chilankhula chi chichewa cha Ku Zambia ndi Malawi / From Wikipedia, the free encyclopedia
Chichewa, (Chicheŵa mu chilankhulo cha ku Malaŵi, chomwe chimatchulidwanso kuti Chinyanja) ndi chilankhulo cha anthu a chi Bantu ndipo chimalankhulidwa kwambiri kummwela kwa dziko la Malawi, ndi kumvuma kwa dziko la Zambia. Mau oyamba okuti Chi- amene amalembedwanso kuti Ci- amatanthauza “mokhala ngati”, motero liu loti Chichewa limatanthauza “mokhala ngati Achewa”, choncho chilankhulochi chimadziwikanso ndi maina okuti Chewa kapena Nyanja. Chingoni (Ngoni) ndi Chikunda (Kunda) ndi kalankhulidwe kena ka chilankhulochi. Ena mwa ma Liu a mchichewa afanananso ndi Shona, isizulu ndebele komanso Isixhosa.